| Lyrics: | 1.
Mlungu dalitsani Malawi,
Mumsunge m'mtendere.
Gonjetsani adani onse,
Njala,
nthenda, nsanje.
Lunzitsani mitima yathu,
Kuti tisaope.
Mdalitse Mtsogo leri na
fe,
Ndi Mai Malawi.
2.
Malawi ndziko lokongola,
La chonde ndi ufulu,
Nyanja ndi
mphepo ya m'mapiri,
Ndithudi tadala.
Zigwa, mapiri, nthaka, dzinthu,
N'mphatso
zaulere.
Nkhalango, madambo abwino.
Ngwokoma Malawi.
3.
O! Ufulu
tigwirizane,
Kukweza Malawi.
Ndi chikondi, khama, kumvera,
Timutumikire.
Pa nkhondo
nkana pa mtendere,
Cholinga n'chimodzi.
Mai, bambo, tidzipereke,
Pokweza
Malawi.
Sent by Carlos Andr Pereira da Silva Branco |